Wadzozedwa Zonyera Zambuzi


Kudzodzedwa- Malawi24
“Hawu! Hawu! Hawu! Weza Nayo!” Iyo idali mfuu ya angoni omwe Loweruka adasonkhana m’boma la Dedza kukachitira umboni kudzozedwa kwa Zonyera Zambuzi.

A Enoch Zonyera Zambuzi Kalapino, adzozedwa mwachikhalidwe cha Angoni kukhala iNkosi Kachindamoto VIII m’boma la Dedza.

A Zonyera omwe ali ndi zaka 61, awadzodza kutsatira imfa ya a Tereza Kachindamoto ndipo mwambowu unachitikira ku likulu la ufumuwu ku Nkosini ku Mtakataka m’bomali.

INkosi ya Makhosi Gomani, omwe pachikhalidwe amatchedwa kuti Ngwenyama, ndiwo alonga ufumu a Zambuzi Kalapino potengera kuti ufumuwu ndi gawo limodzi la Angoni a mtundu wa Maseko.

Mlembi wamkulu ku bungwe la Maseko Ngoni Heritage Trust iMpi Kandi Padambo anati mwambo wa lero unali osiyana ndi omwe boma limkalonga mfumuyi kubwalo la zamasewero la Dedza m’mwezi wapitawo.

Padambo anafotokoza kuti mwambo omwe unachitikira pabwalo lazamasewero la Dedza unali chabe mwambo wopereka mwinjiro wachifumu motsatirana ndi ndondomeko ya boma.

Iye anati lero ndi tsiku lomwe amalonga kapena kuti kudzoza mwachikhalidwe chawo ndipo izi zimayenera kuchitikira pa phata la namwaliyo komanso umachitikira m’khola kutengera ndi chikhalidwe chawo.

Apa a Padambo anati izi sizikadatheka ku mwambo omwe udakonzedwa ndi unduna wa zamaboma aang’ono ndi chitukuko ku bwalo la zamasewero la Dedza potengera kuti patsikulo mwambowu udachitikira mophatikizana ndi mafumu a mitundu ina.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading