Boma ili ndi la MCP langosiyana kuti ili lalawirira kuba — Usi


Usi

Atakhala nthawi osayankhula ku gulu, yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Michael Usi, watsotsomola moto pomwe wati DPP ndi MCP ndi mapasa, chabe kuti winayo walawirira kusolola.

Usi yemwe ndi mtsogoleri wa chipani cha Odya Zake Alibe Mulandu, wati kusiyana kokhako komwe kulipo pakati pa ulamuliro wa DPP ndi wapitawu wa MCP ndikoti wapanowu walawirira katangale ndi kuba chuma cha boma.

Poyankhula ndi imodzi mwa nyumba zofalitsa m’dziko muno, Usi wati Tonse Alliance inayamba bwino itapambana zisankho za 2020, koma zinthu zinayamba kusolobana pomwe MCP imachita litima poyika kunja atsogoleri a zipani zina kuti asalamulire nawo.

Usi amayankhapo pa fuso la mmene boma la DPP layambira kwa chaka chimodzi kuchokera pomwe linatenga ulamuliro potsatira chisankho cha pa 16 September 2025.

“Tonse inayamba bwino mpaka pomwe MCP inayamba kusenda zipani zina kuti zisalamule nawo, koma awa alawirira kuba,” anatero Usi.

Usi watiso palibe chifukwa choti DPP idzinyadira kuti anthu akudya kamba koti ndizinthu zachidziwikire kuti munthu amafunika kudya kuti akhale ndi moyo.

Iwo ati chofunika kwambiri ndikuthetsa katangale ndi umbanda komaso kupanga chitukuko osati kumakamba nkhani zakudya.

“Alipo angaloledwe ndi mkazi chifukwa cha mfundo yoti udzikadya, ndizinthu zachidziwikire kuti munthu ayenera kudya kuti akhale ndi moyo”

Wachiwiri wakale wa mtsogoleri wa dziko linoyu anapemphaso anthu andale kuti adziwopa anthu wamba akamachita zinthu zawo

Apa Using wati anthu wamba ndi omwe amakhala ndi mphamvu yolemba kapena kuchotsa munthu pa udindo.

Kumbali ya zabwino zomwe DPP yapanga kwa chaka chimodzi, a Usi ati angoonapo kusapezeka kwa “Ana Adadi” othe andmwe ankazuza anthu mu ulamuliro wa chipanichi omwe unagonja ku Tonse Alliance mu 2019.

A Michael Usi alangiza DPP kuti ikonze maka posiya katangale komaso kukweza miyoyo ya anthu mdziko muno, ndipo ati malangizowa ndiwofunira zabwino ulamulirowu osati kuwunyazitsa kapena kufuna kuugwetsa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading