Ndidzayesetsa MCP isadzapeze MP ku Ntcheu — Chisale


Normanchisale- Malawi24

Ngati chipani cha MCP chikukhumbira kudzapeza phungu m’boma la Ntcheu pa chisankho cha 2030, chikuyenera chivale dzilimbe pomwe m’modzi wa aphungu m’bomali wabetchera kuti izi sizidzachitika.

Phungu wa dera lapakati m’boma la Ntcheu, Norman Chisale walonjeza kuti adzachita chilichonse, ngakhale kufika posauka, kuti chipani cha Malawi Congress chisadzapeze phungu wa nyumba yamalamulo m’boma lonse.

Poyankhula pa msonkhano ku dera lake, Chisale anati ndiwokhumudwa ndi mmene Congress inamuzunzira kuphatikizaso anthu ena aku Ntcheu.

“Ngati tili ndi m’dani wa mkulu wa boma lonse la Ntcheu ndi Kongeresi, ndipo ndidzalolera kuphulitsa nsapato zanga ineyo nkukhala osauka koma ku Ntcheu kuno sadzapezako phungu wa nyumba yamalamulo, sizidzatheka” watero Chisale.

Iye wati adzapanga izi potsatira nkhaza zomwe chipani cha Kongeresi chinamuchitira.

Chisale anatchula kumangidwa kwake miyezi isanu ndi umodzi pomwe Kongeresi inkalamulira, komaso nkhaza zomwe mneneri ochokera ku Ntcheu, Shepherd Bushiri ndi mwana wa mtsogoleri wa dziko lino, Tadikira anakumana nazo nthawi ya Kongeresi.

Phunguyu anati anthu onsewa analandira nkhanza ndi nkhani zongopeka, koma anati wakhululukira aliyese yemwe anachita izi.

“Munthu oyambilira kumukhululukira ndi Steven Kayuni yemwe anathawa m’dziko muno, ndikanakhala kuti ndimafuna kuthana naye zikanatheka koma akamuweruze ndi Mulungu. Mnyamata ameneyotu anatizunza, si ine ndekha komaso

“Bushiri m’bale wathu wamu Ntcheu muno anakaniza mwana wake kupita kuchipatala mpaka anamwalira, komaso Tadikira anamusunga kundende miyezi isanu ndi umodzi nkhani zabodza,” wateroso Chisale.

Norman Chisale anati zimamuwawa McP ikamazunza anthu aku Ntcheu ndipo anachenjeza chipanichi kuti kakhale komaliza kuchita mchitidwewu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading