CRFA yamaliza kampeni ku Ntcheu

Advertisement
Central Region Football Association (CRFA)

Akuluakulu kuchokera mu komiti yoyendetsa masewero a Mpira wamiyendo mchigawo chapakati ya Central Region Football Association (CRFA), amaliza kuchita kampeni ku mazoni a m’boma la Ntcheu, yomwe cholinga chake ndikugwetsa utsogoleri omwe ulipo pano m’bomali.

Msungichuma wa CRFA, Hastings Chilunga anatsogolera ma membala anayi a bungweli, Joe Twaibu, Tseka Jickson Aluya komaso Paul Kampira pa ulendo wawo waku Ntcheu.

Malingana ndimalipoti, nthumwizi zinayambila kuyima kwa Njolomole koma anasemphana maganizo ndi utsogoleri kumeneko pomwe unakana ganizo la CRFA loti asadzavotere wapampando wapano Williams Kapenuka pazisankho.

Nthumwizi zinakumanaso ndi zoni yapa Ntcheu-boma kenaka ku Msipe komwe anakumana ndi mlembi kumeneko.

Iwo sanasiyile pomwepo koma kupitaso ku Chimatu, Manjawira, Bilira mpaka kukamalizila zoni ya Kasinje.

Izi zikudza pomwe pali kusamvana pakati pa CRFA komaso komiti ya masewero a mpira wamiyendo ku Ntcheu.

Kusamvanaku kunabwera pomwe CRFA inalepheretsa zisankho ku Ntcheu ponena kuti zoni ya kwa Njolomole sinapatsidwe zikalata zosankhira anthu omwe akuwafuna kuti ayimile pazisankhozi.

Koma patatha tsiku limodzi, Zoni ya Njolomole inatsutsa zomwe CRFA inanena polepheretsa zisankhozi ndipo inati, iwo anatsatila ndondomeko zonse zoyenela.

Titafusa wapampando wa komiti ya Ntcheu, Williams Kapenuka anawulura kuti zonsezi zikuchitika kamba koti anthu omwe imafuna CRFA, sanasankhidwe kuti adzayimile nawo pazisankhozi.

Iye anaulura kuti mlembi wamkulu wa CRFA, Antonio Manda analonjeza zothana ndi komiti ya Ntcheu, kamba koti sinamusankhe kuti adzapikisane nawo pa zisankho za CRFA, zomwe Manda anapambana miyezi yapitayi.

Pakadali pano anthu osiyanasiyana adzudzula mchitidwe wa Manda, osalemekeza zofuna za anthu aku Ntcheu.

Ena ati zonsezi zikuchitika mwadala, ndicholinga choti pakafika pa 30 Epulo, pomwe CRFA inayika ngati tsiku lotsiliza kusankha atsogoleri mmaboma achigawo chapakati, bungweli lidzathetse komiti yomwe ilipo pano ku Ntcheu ndikusankha yawo yogwirizila.