
Mwambi woti tsoka likalimba amakuluma ndi galu wako yemwe wapherezeka lero mnyumba ya malamulo pomwe phungu wa chipani cha Malawi Congress (MCP), Yona Mkandawire wadera la Rumphi West, wazukuta bajeti ya 2025-2026 m’nyumbayi ndikunena kuti ndi bajeti yosakaza ndalama m’malo mopanga ndalama.
Phunguyi wati ndizokayikitsa ngati dziko lino likwanitse masomphenya ake a 2063 ndi bajetiyi.
“Bajetiyi siithandiza aMalawi, m’malo moti boma liyike mphamvu zake potsegula ma fakitale ndi ndondomeko zina likutaya ndalama zambiri, m’malo mopanga invest, ” anatero Mkandawire.
Iwo adatsindika kuti kulephera kwa boma kuzenga anthu okhudzidwa ndi milandu ya ziphuphu ndi katangale ndivuto lina lomwe likuchedwetsa chitukuko cha dziko.
Aka sikoyamba kuti Mkandawire abwere poyera ndikutsusana ndi maganizo achipani chake. Iye anali woyamba kunena kuti SONA yomwe mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anapereka m’nyumbayi zambiri mwa izo zinali zabodza.