
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Michael Usi lero anyamuka ulendo opitanso mdziko la Namibia kukakhala nawo pa mwambo olumbilitsa mtsogoleri watsopano wa dzikolo a Netumbo Nandi-Ndaitwah.
Malinga ndi chikalata chochokera ku unduna wowona za maubale a dziko lino ndi mayiko ena, mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ndiwo atuma a Usi kuti akawayimilire m’malo mwawo, ndipo achita kuitanidwa ndi mtsogoleri wa dzikolo amene akulamulira pakali pano.
Mwambo olumbilitsa a Ndaitwah uchitike mawa pa 21 March mu mzinda wa Windhock, pomwenso dzikolo likhale likukondwelera zaka 35 za ufulu odzilamulira.
A Usi akuyembekezeleka kubwelera kuno kumudzi loweluka pa 22 March 2025, nthawi ya kumasana kudzera pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe
Kumapeto kwa mwezi wa February a Usi anakayimiliranso mtsogoleri wa dziko lino pa mwambo wamaliro a tate wa dziko la Namibia a Sam Nujoma omwe unachitikiranso mu mzinda wa Windhock.
Akalumbilitsidwa a Nandi-Ndaitwah omwe anababwa pa 29 October 1959 ndipo amatchuka ndi dzina loti NNN akhala mzimayi oyamba kukhala mtsogoleri wa dziko la Namibia wa chizimayi pomwe akutenga udindo wa mtsogoleri wa dzikolo m’manja mwa Nangolo Mbumba,