
Zadziwika kuti aphungu ambiri akumajomba ku Nyumba ya Malamulo pamene dzulo aphungu okwana 141 anajomba kunyumbayi. Pa nthawi yoitana mayina m’modzi m’modzi aphungu 51 okha ndi omwe anabwera.
Mtsogoleri wa zokambirana mnyumbayi a Richard Chimwendo Banda anapempha kuti pachitike kaundula wa aphungu omwe anabwera.
Izi zili chonchi, wachiwiri kwa wachiwiri kwa sipikala a Aisha Adams anapempha aphungu kuti achepetse kujomba komanso kuchedwa.
Munkumanowu, Nduna yowona za mphamvu a Ibrahim Matola anati mu ndondomeko yoika magetsi ya Malawi Rural Electrification Program (MAREP-10) ikuyembekezeka kulumikizitsa malo ochitila malonda (trading centres) okwana 700 ngakhale gawo la MAREP -9 sanamalize.
Mwa zina zomwe zinachitika mnyumbayi, phungu wa chipani cha DPP a Sameer Suleman, anauza Nyumba ya Malamulo kuti mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera akuyenera kutula pansi udindo wake chifukwa chowuza anthu bodza panthawi yomwe amatsegulira mkumano wa nyumbayi.