Dziko landivuta kuyendetsa zaka zisanuzi koma mukandivotelanso, mudzananala – Chakwera 

Advertisement
Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati a Malawi adzasangalara mu gawo lachiwiri la ulamuliro wawo omwe uyambe chikachitika chisankho cha dziko cha chaka chino.

A Chakwera avomereza kuti dziko lawavuta kuyendetsa maka mu zaka zisanu zomwe alamulira ndipo a Malawi ochuluka zedi amva kuwawa kwambiri mu ulamuliro umenewu.

Malinga ndi a Chakwera kumva kuwawaku kwadza chifukwa choti boma lawo limakonza zolakwila zomwe boma la DPP linasiya.

Iye amayankhula izi pomwe amalumbiritsa nduna ndi achiwiri kwa nduna zomwe wasankha kuti agwire nawo ntchito.

Chakwera anapitiriza kunena kuti a Malawi ali pa uluru chifukwa cha chithupsa chomwe chakhala chikuzunza a Malawi kwa nthawi yaitali. 

Chithupsachi, malinga ndi a Chakwera, ndi katangale komanso kusakadza ndalama, zomwe zakhala zikuchitika m’dziko muno. 

Koma mu ulamuliro wa a Chakwera katangale ndi kusakadza ndalama mosaganizira a Malawi ovutika ndi zinthu zina zomwe zakhala zikukuchitika ndipo mabungwe ndi mayiko akunja akhala akudzudzula Chakwera ndi boma lake pokanika kuthana ndi katangale.