Bambo wa zaka 29, Yzonie Unyolo, wathilidwa Unyolo ndi apolisi m’boma la Mwanza kamba komuganizira kuti amachita zachisembwere ndi mwana omupeza wa zaka zisanu ndi zinayi (9).
Ofalitsa nkhani za polisi m’boma la Mwanza a Hope Kasakula atsimikiza kuti njondayi ayikwidzinga atatsinidwa khutu ndi mayi ake a mwanayu omwenso ndi mkazi wa bamboyu.
Malingana ndi a Kasakula, chomwe chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke nyanga ndi chakuti mai a mwanayu adachita adadabwa atawona kuti mwana wawo akuvutika mayendedwe.
Kenako, mayiwo akuti adampatsa mwanayu mankhwala ochepetsa ululu ndi chikhulupiliro kuti mwina mwanayu apeza bwino.
Ataona kuti palibe chomwe chikusintha, mayiwo adamupanikiza mwanayo ndi mafunso kufikira pomwe adaulula kuti bamboyo amachita naye masewera aku bedi.
Zitatele, maiwa adakatsina khutu apolisi omwe sadachedwe koma kukwidzinga bamboyu ndi Unyolo.
Malingana ndi a Kasakula, zotsatira za chipatala zasonyeza kuti kupatula kugwililidwa, mwanayu adapatsilidwanso matenda a Chindoko.
Pakadalipano, oganizilidwayu waonekera kale m’bwalo la milandu ndipo mboni zitatu zapeleka kale umboni wake.
Unyolo amachokera m’mudzi mwa Chikolosa, mfumu yaikulu Kanduku m’boma lomweri la Mwanza.