Mponda wati kugonja kwa Civo ndi zokhumudwitsa

Advertisement
Lilongwe Derby

Atakanika kugonjetsa adani awo a mu Lilongwe, mphunzitsi wa Silver Strikers Peter Mponda wati kugonja ndi Civil service United ndi zokhumudwitsa.

Anyamata a ma Banker omwe anayitana anyamata a Civil pa bwalo la Silver mu mzinda wa Lilongwe, mphunzitsi wawo Mponda wati masomphenya sakuchoka ofuna kutenga chikho cha 2024 TNM Super League.

Mponda yemwe timu yake ili pa nambala yoyambilira pa mndandanda ndi ma pointi 51 mu masewelo 23 tsopano ndiyokhayo yomwe sikugonja m’masewelo ndipo wati kutaya ma points lero chisakhale chokhumudwitsa pa anyamata ake.

Wilson Chidati wachiwiri kwa mphuzitsi wa Civil Service United wati anawapatsa mpata anyamata ake kuti amenye m’mene akufunira ndipo wati iwo ukuyang’ana kuthera mu ‘top 4’.

“Anyamata akumenya bwino kwambiri zosiyana ndi m’mene anayambira kumayambiliro kwa mpikisano, izi ndi zolimbikitsa. Ife sitikuyang’ana top 8 tikuyang’ana top 4,” anatero a Chidati.

Mu masewelo achiwiri a sabata ya chi 25 ya chikho TNM Super League zatha motele kuti

  1. Silver Strikers 0-0 Civil Service united
  2. Creck Sporting 0-1 Karonga United
  3. Bangwe All Stars 1-1 Kamuzu Barracks
  4. MAFCO FC 2-1 Baka City

Mpikisano olimbilana ukatswiri wa 2024 udakali wa mphamvu pakati pa Silver Strikers, Mighty Mukuru Wanderers, ndi FCB Nyasa Big Bullets pamene onse atsala ndi masewelo 7 aliyense.

Advertisement