…boma lawaonjezera malipiro ndi 41%
…aloledwa kuitanitsa galimoto osakhomela msonkho
Akakhala oweruza milandu zawo zoyera, za kukokanakokana timaziona ndi anamwino kapena ena oyendetsa galimoto zikulu-zikulu sizinaoneke kwenikweni. Ngakhale iwo eni oweruza milandu ayamika ndi kusintha kwa phindu lomwe azipeza akagwira ntchito tsopano.
Patangotha sabata ziwiri a bwalo ataopseza kuti ayamba kunyanyala ntchito, boma lasintha malipiro ndi phindu lina lomwe a bwalo amapeza pa ntchito yawo. Malinga ndi malipoti, boma lavomereza kukwera kwa malipiro akuluakulu oweruza mu ma bwalo a dziko lino.
Mu ndondomeko ya malipiro atsopanowa, ena a bwalo malipiro awo awonjezeredwa ndi MK21 pa MK100 iliyonse pamene ena awonjezeredwa ndi MK41 pa MK100 iliyonse. Izi zikusiyana ndi momwe anthu ogwira m’boma ena awonjezeredwa ndalama yawo pamene Kwacha inagwa mphamvu. Iwo adaonjezeredwa ndi MK12 pa MK100 iliyonse ngakhale kuti ndalama ya dziko lino idagwetsedwa mphamvu ndi MK45 pa MK100 iliyonse.
Kupatulapo kuwaonjezera malipiro awo a pa mwezi, ati boma lavomelanso kuti onse oweruza milandu ku mabwalo ang’ono ang’ono kapena kuti ma majisitireti azitha kulowetsa galimoto mu dziko muno osalipira msonkho ulionse muja aphungu achitira. Iwo ati aziloledwa kuchita izi kamodzi pa zaka zisanu.
Malinga ndi nyuzipepala ya Nation, akuluakulu olankhulira anthu oweruza ati iwo ndi okondwa ndi zimene boma lachita powakwezera malipiro ndi kuwalola kuti azilowetsa galimoto opanda msonkho. Iwo ati izi zawakondweretsa ngakhale kuti zina mwa zimene amafuna monga kukwera kwa mlingo wa mafuta umene amapatsidwa ndi boma sizinatheke.
Mu dziko muno mwakhala muli madando okhuza malipiro kuchokera kwa anthu ambiri a pa ntchito. Anthu ambiri akhala akudandaula kuti malipiro awo sakukwana kamba ka kukwera kwa zinthu mu dziko muno.