Anthu asanu ndi m’modzi anjatidwa pogenda ma ofesi a nthambi yowona zolowa ndi zotuluka

Advertisement
Immigration

Anthu asanu ndi m’modzi (6) mu nzinda wa Lilongwe, ali m’manja mwa apolisi poganizilidwa kuti anali m’gulu la omwe anagenda ma ofesi a nthambi yowona zolowa ndikutuluka m’dziko muno (DICS) pa nkhani ya ziphaso.

Lachinayi masana, anthu okwiya mu nzindawu anagenda ku maofesi a nthambi ya DISC kamba kokhumudwa kuti nthambiyi ikuchedwa kuwapatsa ziphaso zawo zoyendera zomwe akuti anapangitsa miyezi yapitayo.

Mwazina, anthuwa anagenda ndikuswa magalasi a ofesi za nthambiyi, kutchinga nsewu opita ku ma ofesiwa ndi miyala komaso kugenda ena mwa magalimoto omwe anali pa malopo.

Potsatira kafukufuku yemwe anakhazikitsa kutsatira chipwilikitichi, apolisi ati amanga anthu asanu ndi m’modzi. Woyankhulira apolisi kum’mawa kwa chigawo cha pakati a Foster Benjamin ndiye watsimikiza za kumangidwa kwa anthuwa.

A Benjamin awuza nyumba zina zosindikiza nkhani m’dziko muno kuti ambiri mwa anthu omangidwawa ndi omwe amathandiza anthu akamapangitsa ziphaso zoyendera omwe amadziwika ndi dzina loti madobadoba.

Iwo ati kafukufuku anakali mkati kuti apeze ndikumanga anthu enaso omwe akuganizilidwa kuti anatenga nawo gawo pa chipolowechi. A Benjamin awonjezera kuti apolisi akuchita zonse zomwe angathe kuti athetse mchitidwe wa udobadoba ku nthambiyi.

Anthuwa akuyembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu kuti akayankhe mlandu oyambitsa chisokonezo.

Patsikuli, apolisi analowelerapo poponya utsi okhetsa misozi kuti anthuwa abalalike komaso kuti bata libwelere ku ma ofesi onse a nthambi ya DICS m’dziko muno.

Advertisement