Chakwera waimitsa ulendo wake waku Bahamas

Advertisement
Saulos Chilima

Mtsogoleri wa dziko lino walephera kunyamuka ulendo wake opita m’dziko la Bahamas komaso Switzerland kamba kakusowa kwa ndege yomwe anakwera wachiwiri wake Saulos Chilima.

Kalata yomwe boma latulutsa yomwe wa sainira ndi mlembi wa mkulu wa boma Colleen Kamba, yatsimikiza kuti ndege yomwe inanyamula Chilima ndi anthu ena siikupezekabe mpaka pano.

Kalatayi yati ndegeyi inanyamula Chilima ndi anthu ena asanu ndi anayi ndipo inanyamuka ku Lilongwe lero, Lolemba pa 10 June 2024 nthawi ya 09:17 m’mawa ndipo idalephera kutera pa bwalo la ndege la Mzuzu International nthawi ya 10:02.

Kalatayi yati akuluakulu a za ndege akulephera kulumikizana ndi ndegeyi kuyambira m’mawa mpaka pano. Izi zapangitsa kuti Chakwera alephere kunyamuka ulendo wake wopita ku Bahamas ndi Switzerland.

 “Mkulu wa gulu lankhondo la Malawi Defence Force, General Valentino Phiri, adadziwitsa a Dr Lazarus McCarthy Chakwera za nkhaniyi ndipo mtsogoleri wa dziko linoyu wayimitsa ulendo wake wopita ku Bahamas ndipo walamula mabungwe onse a mchigawo ndi dziko lino kuti afufuze mwachangu komwe kuli ndegeyo,” yatelo mbali ina yakalatayi

Malipoti osatsimikizika akusonyeza kuti anthu ena anawona ndege ina ikugwa mnkhalango ya Raiply ku Mzuzu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.