Kunali kuphuluza chabe, Jetu apepesa potukwana

Advertisement
Musician Jetu from Malawi

Woyimba Jetu yemwe anayika khwimbi la a Malawi m’botolo, wapepesa kamba kotukwana mukanema ina yatsopano. 

Kuyambira Lachisanu, anthu m’masamba amchezo akhala akugawana kanema wina yemwe akuonetsa woyimba wa zaka 72-yu ali ndi mdzukulu wake pomwe amacheza ndi omutsatira ake kudzera pa kanema ya pompopompo (live video) pa tsamba lake la fesibuku.

Macheza ali mkati, Jetu analavula chichewa chosakhala bwino ndipo munkuyankhulako anatchula woyimba nzake Najere wa m’boma la Mulanje. 

Loweluka Jetu kudzera pa tsamba lake la fesibuku lomwe limayendetsedwa ndi omutsogolera ake pa mayimbidwe, wapepesa kamba kakutukwanako ndipo akuti kunali kuphuluza chabe, sichinali chikozero.

Patsambali palembedwa kuti; “Tikufuna tipepese kaamba ka video clip yomwe ikuyenda mmasamba a mchezo yokhuza katswiri wathu JETU yomwe inadulidwa mu live video yomwe timajambula .

“Tikupepesa pa cholakwika chilichonse chodza kaamba ka video clip imeneyi sizinali zadala inali mistake chabe ndipo sitinafune tilakwire aliyense zikomo.”

Jetu wachita izi pomwe ali m’dziko la South Africa komwe anapita sabata latha ataitanitsidwa kuti akaimbe malo angapo pamodzi ndi Zonke Too Fresh komanso Pop Young.

Advertisement

One Comment

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.