Mchitidwe opempha ndalama andale uthe – Tobias

Advertisement
Milward Tobias is a Malawian presidential aspirant

Yemwe akufuna kupikisana nawo pa mpando wa pulezidenti, a Miliward Tobias, ati m’chitidwe opempha ndalama anthu andale ukuyenera kuti uthe potengera kuti ukubwedzeretsa m’mbuyo anthu omwe ali ndi chidwi choyamba ndale makamaka achinyamata omwe  nthawi zambiri nthumba mwawo mumakhala mochepekedwa.

Poyankhura ndi nyumba ino, Tobias ati achinyamata ambiri omwe chidwi chawo chili pa ndale ndi amantha komanso a nkhawa akalingalira zoyamba ndale popedza ndale za dziko lino dzimakomera yemwe ali ndi kangachepe nthumba mwake, chifukwa kupanda kutero ndiyekuti loto lako lodzakhala munthu wa ndale umaiwaliratu.

Iwo adawonjezera kunena kuti ndale zikuyenera kupereka mpata kwa aliyense komanso achinyamata chifukwa ndi gwero la tsogolo lowala lomwe lingapereke chiyembekezo china mdziko muno chifukwa kupanda kutero ndiyekuti anthu omwe angakhale ndi mpata pa nkhani za ndale ndi ankhalakale okhaokha.

“Achinyamata akuyenera kutenga mbali pa ndale pamene ali ndi mphamvu komanso chidwi chifukwa dzikoli lilimmanja mwawo kuti alikonze. Nkhani ya utsogoleri ndi nkhani yotumikira anthu komanso mbali yofuna kusintha zinthu dziko ngati sidzikuyenda bwino, kotero  achinyamata ali ndi danga komanso kuthekera kotero,” Tobias adatero.

Iwo apempha achinyamata kuti pamene apeza mpata oyamba ndale akuyenera kukhala ndi luntha komanso khumbo lofuna kupititsa chitukuko  cha dziko lino patsogolo posatengera gawo komanso mtundu a munthu.

Kopatura apo , Tobias wati aliyense ofuna kuyamba ndale akuyenera kukhala waungwiro komanso ophunzira mokwanira chifukwa choti ntchito yoyendetsa dziko ikufunikira maphunziro okwanira kuti chuma  cha m’dziko chisamalilike komanso chigwiritsidwe ntchito moyenera. 

Iwo ati monga  m’modzi wachinyamata yemwe akufuna kupikisana pa mpando wa upulesidenti, akufuna kulambura njira yomwe achinyamata adzadutse akadzasankhidwa pa mpando popedza izi zidzapangitsa achinyamatawa kuti akhale ndi danga.

Iwo ati a Malawi akuyenera kukhala m’maso komanso kuchenjera pa dzitsankho zikubwerazi kuti adzasankhe mtsogoleri yemwe alindi masophenya osintha zinthu komanso amene adzapereke utsogoleri wokomera aliyense posatengera chigawo kapena chipembedzo cha munthu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.