Zayang’ana kungolo: khothi lati Kalumo sioyenera kutsogolera nthambi ya Immigration

Advertisement
Charles Kalumo

Ogwira ntchito ku nthambi yowona zolowa ndikutuluka m’dziko muno ya DICS akuyenera kukhala osangalala pomwe bwalo la milandu munzinda wa Blantyre lalamula kuti Brigadier General Charles Kalumo asiye ntchito ku nthambiyi kamba koti anasankhidwa mosatsata malamulo.

Malingana ndi kalata yachigamulo yomwe tsamba lino lawona, mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera sanali oyenera kusankha mkulu wa nthambiyi koma nduna ya zachitetezo cha m’dziko.

Kuwonjezera apo, oweruza milandu Mike Tembo wati a Kalumo sanalinso oyenera kusankhidwa pa udindowu kamba koti zaka zake sizikumuyeneleza kukhala pa udindowu malingana ndi malamulo a dziko lino.

“Khoti ili likulamulanso nduna ya zachitetezo cha m’dziko, mogwirizana ndi malamulo oyenerera, kuti apeze munthu wina kulowa pa udindo wa Director General of Immigration and Citizenship Services popeza izi zili m’manja mwa ndunayo.

“Chotsatira chake, Brigadier General Charles Kalumo (Wopuma pantchito) akulamulidwa kuti asiye kugwira ntchito yotsogolera DICS atasankhidwa ndi woyimbidwa mlandu (Chakwera) motsutsana ndi lamulo loyenera,” yatelo mbali ina yachigulochi.

Chikhulupiliro Zidana ndiyemwe adakadandaula za nkhaniyi ku bwalo la milandu ponena kuti Kalumo anasankhidwa mosatsata malamulo.

Izi zikudzapomwe ogwira ntchito ku nthambi ya DICS anapeleka masiku khumi kwa Kalumo kuti atule pansi udindo wake ponena kuti mkuluyu walephera kutsogolera nthambiyi.

Kumayambiliro kwa sabata ino, ogwira ntchito ku nthambiyi analengeza kuti kuyambira lero Lachinayi akhala akunyanyala ntchito pofuna kukakamiza Kalumo kutula pansi udindo.

Kunyanyala ntchitoku kwelepheleka kamba ka kalata yomwe boma kudzera ku unduna wa zachitetezo cha m’dziko inatulutsa yowopsyeza kuti kunyanyala ntchito ku ma ofesi a nthambiyi ndikoletsedwa. 

Advertisement