Ophunzira 9,226 awasankha kukachita maphunziro msukulu za ukachenjede khumi ndi imodzi

Advertisement
MUBAS

Unduna wa Zamaphunziro watulutsa m’ndandanda wa mayina a ophunzira omwe asankhindwa kukachita maphunziro awo osiyanasiyana m’ma yunivesite a boma. Ophunzira okwana 9,226 ndi omwe asankhidwa pa ophunzira okwana 19, 250 omwe adalembera.

Malingana ndi kalata yomwe undunawu watulutsa ndipo wasayinira ndi mlembi wamkulu Mangani Chilala Katundu, mafomu okwana 17,906 ndi omwe adakwanilitsa zonse zofunika pa mafomu okwana 19,250 omwe adalembera.

Katundu wati pa ophunzira 9,226 omwe asankhidwa kukachita maphunziro awo ku yunivesite, 5,326 ndi amuna, kuyimilira 57.7 peresenti pamene 3,902 ndi aakazi kuyimilira 42.3 peresenti.

Ma yunivesitewa ndi Mzuzu University (MZUNI), Kamuzu University of Health Sciences (KUHES) Lilongwe University of Agriculture (LUANAR), Malawi University of Business and Applied Sciences (MUBAS), University of Malawi (UNIMA), komanso Malawi University of Sciences and Technology (MUST).

Kuphatikiza apo iye wati ophunzira okwana 1896 awasankha kukachita maphunziro awo ku sukulu za ukachenje zosula aphunzitsi za Nalikule ndi Domas.

Malingana ndi mlembiyu, ophunzira ophunzira omwe awasankha ku Nalikule ndi Domas, ophunzira 994 ndi aamuna kuimira 52.4. peresenti pamene 902 ndi akazi kuimira 47.6.

Pakadali pano, omwe adalembera nawo izi awapatsa masabata atatu kuti apereke madando awo pa zokhudzana ndi chisankhocho. 

Ntchito yosankhira ophunzira msukulu zaukachenjede m’dziko muno imayendetsedwa ndi bungwe la National Council for Higher Education (NCHE).

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.