Mumangidwa mukanyanyala ntchito – boma lawopseza maofesala ku nthambi yowona zolowa ndi zotuluka

Advertisement
Malawi Immigration offices in Lilngwe

Boma lawopseza kuti ogwira ntchito ku nthambi yowona zolowa ndi kutuluka ya DISC omwe akufuna kunyanyala ntchito kuyambira lero, amangidwa ponena kuti kunyanyala ntchitoku nkosaloredwa ndi malamulo.

 Kumayambiliro kwa sabata ino, ogwira ntchito ku Department of Immigration and Citizenship Services (DICS) analengeza kuti kuyambira lero Lachinayi akhala akunyanyala ntchito pofuna kukakamiza kuti mkulu wa nthambiyi a Charles Kalumo atule pansi udindo wawo.

Koma boma kudzera mu kalata yomwe wasainira ndi mlembi wa unduna wa zachitetezo cha m’dziko a Steven Kayuni, kunyanyala ntchitoku ndikosaloledwa ponena kuti ogwira ntchitowa sanatsate ndondomeko zoyenera pa chilinganizo chawochi.

Mu kalatayi, a Kayuni ati ma ofesi onse a nthambiyi akhala otsekula monga mwa nthawi zonse ndipo ati lamulo ligwira ntchito pa ogwira ntchito onse omwe akhale akunyanyala ntchito.

“Kunyanyala ntchito kukunenedwaku ndikosaloledwa kamba koti sipanakhalepo kutsatira njira zokhazikitsidwa ndi lamulo. Unduna sunyalanyaza kugwiritsa ntchito lamulo lololedwa.

“Unduna wa zachitetezo ukuchenjeza maofesalawa kuti kukhala maofesala ku DICS kenakaso ndi kunyanyala ntchito, ndi kuphwanya malamulo ndipo zili ngati kukonza chiwembu. Amene angamangidwe pa izi, pali chilango chokhala m’ndende zaka zingapo,” watelo Kayuni mu kalatayi.

Ogwira ntchito ku nthambiyi akuloza chala Kalumo pakusayenda bwino kwa nthambi ya DICS. Mwa zina iwo ati Kalumo alibe upangili wa utsogoleri zomwe akuti zikuchititsa kuti ntchito ku nthambiyi isokonekele kwambiri.

Pakadali pano sizikudziwika ngati ogwira ntchito ku nthambiyi apitilire ndi chilinganizo chawo chonyanyala ntchito potsatira chiopsezochi. 

Advertisement