Chilomba wasankhidwa ogwirizira udindo wa mkulu wa ACB

Advertisement
Hillary Chilomba - ACB

Wofalitsa nkhani ku bungwe lolimbana ndi katangale la ACB a Egrita Ndala ati a Hillary Chilomba yemwe anali wamkulu wachiwiri ku bungweli tsopano ndi omwe akhale akugwilizira ngati wamkulu kutsatira kutha kwa kontalakiti ya a Martha Chizuma.

Wofalitsa nkhaniyu wanena izi kudzera m’chikalata chomwe bungweli latulutsa ndipo ati izi zachitika mogwilizana ndi gawo 8 loyendetsera milandu ya katangale.

Pofuna kuti ntchito yolimbana ndi katangale ipite patsogolo, iwo apemphanso magulu onse okhudzidwa kuti agwirane manja ndi a Chilombo kuti izi zitheke.

Kontalakiti ya a Chizuma yemwe adali wamkulu ku bungweli inatha pa 31 May Chaka chino.

Ndala wayamikiranso a Chizuma kamba kantchito yabwino yomwe anagwira yolimbana ndi katangale mdziko muno.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.