A Chilima ali m’dziko la Korea ku m’kumano wa Korea ndi maiko a muno mu Africa

Advertisement
Vice President Saulos Chilima

Wachiwiri kwa m’tsogoleri wadziko lino a Saulos Chilima, ali m’dziko la Korea komwe akuyimilira dziko lino ku nkumano omwe watsekulidwa lero wotchedwa Korea-Africa Summit omwe ukuchitika m’dzikolo.

Cholinga chachikulu cha msonkhanowu ndikufufuza mwayi wamalonda ndi zachuma pakati pa dziko la Korea ndi mayiko amuno mu Africa.

Wachiwiri kwa m’tsogoleri wadziko linoyo ali ku msonkhanowu ngati nthumwi yoimilira mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.

Ndalama zankhaninkhani zokwana madola 24 biliyoni  ndizomwe zikuyembekezeka kuperekedwa pa msonkhanowu ndi dziko la Korea

Mayiko amuno mu Africa oposa 50 ndi omwe afika ku msonkhanowu kukakhala nawo pa zokambiranazi.

Wachiwiri kwa mtsogoleriyu akuyembekezeka kubwelera kuno ku mudzi lachisanu likudzali pa 7 June.

Aka ndi kachiwiri kuti a Chakwera atume a Chilima kukawaimilira ku zochitika za dziko lino ku maiko akunja chiwaletseleni kuchita izi ati kamba kowaganizira kuti adapanga zakatangale ndi mzika ya Britain a Zunneth Sattar m’buyomu, mlandu omwe mkulu oyimilira boma pa milandu a Madalitso Chamkakala adauthetsa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.