Watha vinyo mwa Pasuwa: nawo maule achapidwa ndi Siliva

Advertisement
Silver Strikers beats Nyasa Big Bullets

A Nyerere atha kunamizila kuti anachapidwa koyenda, koma maule ndiye aswedwa pamaso pa akazi awo ndi apongozi awo. Pakwawo pompo awonetsedwa mbonaona. Ndi kutheka kuti ligi ija nawo sayionanso. Peter Mponda sanabwere kugawa ma suwiti.

Tsogolo la Silver Strikers mu ligi ya TNM likunkera likuwalira pamene lero athibula msungi ligi Nyasa Big Bullets pa bwalo la Kamuzu stadium mu mzinda wa Blantyre. Pa masewero amene anakola chidwi cha anthu okonda masewero mu mzinda wa Blantyre komanso Malawi yonse, inali nthawi yoti mphunzitsi Peter Mponda amakumana ndi timu yake yakale.

Timu ya Bullets inayamba ndi kuopseza, kuonetsa ngati achita zakupsa, koma nyonga zawo zonse zinanka kupita pachabe pamene nawo ma Banker anaonetsetsa kuti cholinga chawo ndi choti atsomphole ligi ulendo uno.

Anyamata a Bullets monga Patrick Mwaungulu, Precious Phiri ndi Stanley Billiat anatangwa kuonetsa luso lawo koma goloboyi wa ma Banker George Chikooka adapitiriza kuonetsa chikoka chake pagolo pokaniza maule kudutsa. M’mene chimatha chigawo choyamba ndiye kuti adakali chimodzimodzi.

Mu chigawo chachiwiri, ma timu adabwela ndi nzeru za tsopano koma sikuti zidaphula kanthu kwenikweni. Idapitilira kukhala ngati ndewu ya zitsiru, yopanda phindu kwenikweni. Ena mpaka adayamba kuvomera kuti basi alepherana ndiye kuti a Bullets aziti bola iwo sanamenyedwe kusiyana ndi nyerere.

Koma amene adanena kuti mpira ndi 90 yonse nkulinga ataona chifukwa pamene a Bullets amati kwalero kwatha, angodikila nthawi yoonjezera, pompo ndi pamene adalatsidwa mu nthiti ndi ma Banker. Chinsinsi Maonga ndiye adatulutsa muvi omwe udalatsa nthiti ya maule, kudzetsa chisoni kwa aja amazitcha kuti n’kumadzulo.

M’mene oyimbila amathetsa ndiye kuti Silver Strikers ikunyadila kuti yakolola ma pointi onse atatu pomwe anzawo a Bullets manja m’khosi, kuswedwa pakwawo pomwe.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.