Mtsogoleri wa gulu la Mzika Zokhudzidwa Edward Kambanje wamangidwa

Advertisement
Edward Kambanje

M’tsogoleri wa gulu la Mzika Zokhudzidwa a Edward Kambanje wamangidwa kamba ka kalata yomwe analembera bungwe la ACB kuti lifufuze kapezedwe ka galimoto 20 zomwe nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda anagulira mwana wawo momwe akuti munali siginetcha ya membala wa gululi yemwe pano wakana kuti sanasayinire nawo kalatayi.

M’modzi mwa akuluakulu a gululi a Osman Tagiya watsimikizira tsamba lino kuti Kambanje wamangidwa Lachisanu pa 31 May 2024 cha m’ma 7 koloko usiku mu nzinda wa Blantyre.

Tagiya watiuza kuti apolisi amanga Kambanje pomuganizira kuti anagwilitsa ntchito siginetcha ya Queen Kapalamula mopanda chilolezo mu kalata yomwe gululi linalembera bungwe lothana ndi katangale komaso ziphuphu la Anti Corruption Bureau.

Iye wati gululi ndilodabwa kuti Kapalamula yemwe akuti ndi membala wa gulu lawo anauza anthu kuti iye sanatenge nawo gawo polemba kalatayo komanso kuti siginetcha yake inagwilitsidwa ntchito mopanda chilolezo chake.

Tagiya wapempha anthu kuti asakhale ndi mantha pa kumangidwa kwa Kambanje ndipo wanenetsa kuti gulu lawo lipitilira kuyankhula pa zinthu zonse zomwe zisakuyenda bwino m’dziko muno.

“Izi zimakonda kuchitikira anthu omwe akúmenyera ufulu nde tikupempha kuti tigwirane manja tisafooke, tisaope. Zinthu zikalowa ndale zimakhala zovuta.

“Ife sitikhala ndi mantha chifukwa siife oyamba kumangidwa pa nkhani ngati zimenezizi. Ife tilimba mtima mpaka chilungamo pa madandaulo athu chidziwike,” watelo Tagiya.

Sabata ino, Kambanje wakhala akuyendera malo olembetsera ziphatso za umzika munzinda wa Blantyre potsatira mphekesera zoti kukumachitika za chinyengo.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.