A Chakwera akana kuwapaka kukwera mitengo kwa katundu

Advertisement
Lazarus Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati mitengo ya zinthu mdziko muno imapitilira kukwera kwambiri chifukwa boma linagulitsa makampani a boma omwe amatha kuchititsa kuti dziko lidzipeza ndalama zambiri kuti katundu adzikhala ndi mitengo yokhazikika.

Poyankhula  pa mwambo otsekulira Magwero Industrial Park m mzinda wa Lilongwe a Chakwera ati mu chaka cha 1994 andale ndi ena a boma anagulitsa ma Kampani a boma ndipo izi  anachita si iwo ayi, ndipo ati amene anachita izi achite manyazi lero.


Lazarus Chakwera
Sindidakweze katundu ndine – Chakwera.

Iwo anawonjezera kuti nkulakwa kumanena kuti katundu akukwera mitengo chifukwa cha iwo, ndipo ati iwo akhalabe kalikiliki kubwezeletsa ma fakitale amene abwezeretse chuma mdziko muno.

“Wina akamanama kuti wakweza mitengo ya zinthu ndi Chakwera ameneyo achite manyazi chifukwa n’nagulitsa ma Kampani opanga sugar siine, ma Kampani opanga zovala, Malawi savings bank siine ayi, kutseketsa ma fakitale ogulitsa katundu sinnali ine,  timvane nthawi yolimbana ndi amene anabweretsa matenda amenewa ndilibe, nthawi ndilinayo ine  ndi yobwezeletsa ma Kampani ndi ma fakitale,” atero a Chakwera.

M’mawu awo nduna ya zamalonda a Sosten Gwengwe analimbikitsa anthu kuti mkofunika kuti aMalawi ambiri adzikonda katundu opangidwa komkuno ndipo anati Magwero industrial park ipindulira aMalawi ambiri kupeza ntchito komanso ndalama zakunja.

Ntchito iyi yokhazikika malo omanga opangila zinthu a Magwero industrial Park ndi oyamba ndipo ichitika mu zigawo zonse za dziko lino ndi thandizo la ndalama zokwana 1 trillion kwacha kuchokera ku Afrexim Bank.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.