Jetu waotcha mtambo

Advertisement
jetu

“Ambuye wazatheka bwanji”; ngati nkhani ya Sarah mu bayibulo yemwe anabereka mwana atamera kale imvi, woyimba Jetu wakwera ndege kachiwiri pomwe watuluka m’dziko muno koyamba ali ndi zaka 72 kupita kokavinitsa anthu m’dziko la South Africa.

Jetu, yemwe dzina lake lenileni ndi Christina Malaya, pamodzi ndi omuthandizira wake Emmu Dee, anyamuka lero chakum’mawaku kupita m’dziko la South Africa kudzera pabwalo la ndege la Chileka munzinda wa Blantyre.

Woyimbayu limodzi ndi Pop Young komaso Zonke Too Fresh, akuyembekezeka kukasangalatsa anthu ndi mayimbidwe kudera la Cape Town, Johannesburg komanso Randburg m’dziko la South Africa.

Polemba pa tsamba lake la fesibuku, Jetu wasonyeza kusangalala kwambiri kuti loto lake lopita m’dziko la South Africa latheka ndipo wati ndiokondwa kuti kumeneko akakumana ndi mwana wake patatha zaka 14 asanaonane.    

“Zikomo kwa aliyese watengapo gawo kukwanilitsa maloto anga. Pano kwatha zaka zambirimbiri ndisanakumane ndi mwana wanga koma lero ndikupita ku theba komwe ndikakumane naye … Ambuye akudalitseni nonse SOUTH AFRICA celebu wankulu akubwela konko.. anjira Dorothy Kingston – Cashie Madam ambuye akudaliseni,” anatelo Jetu pa tsamba lake la fesibuku.

Kampani ya za nsangulutso ya Chichi Beauty Parlour and Entertainment ndiyomwe yaitanitsa oyimbayu m’dziko la South Africa mothandizana ndi The New Dawn Lodge, Star Travel, Pikho Farms, BBs Car Rentals komaso Eagles Real Estate Consultants.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.