Katangale wachuluka ku nthambi yogura ndi kugulitsa katundu wa boma – Cdedi

Advertisement
CDEDI says Malawi not benefiting from Malawian Airlines, Greenbelt Authority

Bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI) lati m’chitidwe wakatangale ku nthambi yogura ndi kugulitsa katundu wa boma ya Public and Disposal of Assets Authority (PPDA) wamanga nthenje ndipo Boma likuyenera kuwunika komanso kuthetsa m’chitidwewu madzi asanafike m’khosi.

Mkulu wa bungweli, Sylvester Namiwa, wanena izi lero pa msonkhano wa atolankhani omwe unachitikira mu mzinda wa Lilongwe.

Namiwa wati kafukufuku yemwe bungweli lapanga akuonetsa kuti ngakhale nthambiyi imalimbikitsa anthu pa ntchito yogura katundu wa boma kutsata malamuro, sikuwunika ndi chidwi ntchito yogulitsa katunduyu  zomwe zimapatsa mwayi anthu omwe amagwira ntchito yogulitsa katundu wa boma kuti azichita momwe akufunira.

Izi zadziwika pamene Cdedi inalandira madandaulo kuchokera pa malonda a okoshoni omwe anachitika ku likulu la Lilongwe Water Board (LWB), pa 27 April,2024, pomwe amagulitsa katundu yemwe m’modzi mwa iwo ndi galimoto  yaikulu ya mtundu wa Hino 500 truck, registration 5 SC 53, kuti sanatsate malamulo pogulitsa galimotoyi.

“Poyankhapo pa madandaulowa, bungwe la Cdedi linagwiritsa ntchito lamuro lopeza nkhani mosavuta la Access to Information Act (ATL), ndipo tinalembera Kalata mkulu wa bungwe la LWB a Sili Mbewe kuti atiyankhe pa nkhaniyi makamaka momwe kampani ya KADO Auctioners anaisankhira kuti ikhale yomwe igulitse katundu wa LWByu.

“Kupatura apo, timafuna abweretse poyera ndondomeko ndi malamulo omwe anagwiritsa ntchito komanso kuti abweretse poyera lisiti ya ndalama zokwana 10 Million kwacha lomwe analembera munthu yemwe anagura truck yo,” anafotokodza motero Namiwa.

Mkulu wa bungwe la Cdediyu wati LWB kudzera m’chikalata chomwe anawalembera a Mbewe,  anasiyira ntchito yogulitsa galimotoyo a KADO Auctioneers  omwe anagulitsa truckyo kwa munthu yemwe anatchula ndalama zokwana 10 Million, m’malo mogulitsa kwa yemwe ankafuna kugura galimotoyi pa mtengo 15 Million.

Kupatura apo , Namiwa ati kampaniyi ngakhale inaitanitsa anthu okwana asanu kuti akachite okoshoni galimotoyi pa 11 May, anali atalembera kale notice pa 30 April, 2024, yosonyeza kuti omwe achita mphumi ndi a Fabiano Mneyi zomwe zapangitsa a Cdedi kupempha nthambi ya PPDA kuti ilowelelepo komanso kuletsa kampaniyi kuti lisagulitsenso katundu wa boma kufikira nkhaniyi itaunikidwa.

Pomaliza, Cdedi yapempha nthambi yapadera yolimbikitsa kuti malamuro onse oyendetsera kagwiridwe ntchito zosiyanasiyana akutsatidwa pa ntchito zoguritsa katundu wa boma, pofuna kuthana ndi mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.