Luanar ikuyesa mbewu ya chimanga chopilira kumbozi

Advertisement
Maize

Pali chiyembekezo choti zaka ziwiri zikudzazi, dziko la Malawi litha kukhala ndi mbewu yachimanga chopilira ku mbozi komaso mavuto ena pomwe sukulu yaukachenjede ya LUANAR yati ntchito yoyesa mbewuyi ikuyenda bwino.

Akatswiri a sayansi pa sukulu ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources anapanga mbewu ya chimanga yomwe pachingerezi ikumatchedwa biotechnology (bt) Maize yomwe ndiyosiyana ndi mbewu ya chimanga yomwe dziko lino lili nazo.

Lyson Kampira
Cholinga cha maphunzirowa ndi kusula atolankhani pakalembedwe ka nkhani za sayansi – Kampira

Poyankhula pa maphunziro omwe bungwe la National Commission for Science and Technology (NCST) linakonzera atolankhani Lachiwiri munzinda wa Blantyre, mphunzitsi pa sukulu ya LUANAR, Professor James Bokosi anati pano sukuluyi ikuyesa mbewuyi m’madera angapo.

Professor Bokosi ati pali chiyembekezo choti ntchito yoyesa mbewuyi idzafika kumapeto pakutha pa zaka ziwiri zikudzazi kamba koti ikuyenera iyesedwe m’madera osiyanasiyana m’dziko muno.

“Tikuyesera mbewu ya chimanga chomwe ndichopilira ku mbozi. Izi ndi kamba koti panopa sitinapeze njira yothanilana ndi tizilombo timeneti. M’mene tapanga chaka chino ndekuti chaka chamawa tikhala tikukayesaso ku dera kwina kuti tioneso ngati kumeneko chingakhaleso bwino,” watelo Bokosi.

Iye anati “biotechnology” itha kuthandiza kuthana ndimavuta osiyanasiyana okhudza ulimi m’dziko muno monga ng’amba zomwe wati zingathandizire kuti dziko lino lidzikolora chakudya chochuluka chaka ndi chaka.

M’mawu ake pakutha pa maphunzirowa, m’modzi mwa akuluakulu a bungwe la NCST a Lyson Kampira, ati maphunzirowa anawapanga ndicholinga chofuna kusula atolankhani pakalembedwe koyenera ka nkhani za sayansi.  

A Kampira ati chiyembekezo cha bungwe la NCST ndichakuti atolankhani akhala patsogolo kufotokozera anthu ena m’dziko muno zomwe bungwe la NCST likuchita.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.