FIFA yawona oyimbila Nkhakananga

Advertisement
Godfrey Nkhakananga

Bungwe lowona masewelo a mpira wa miyendo pa dziko lonse la FIFA lasankha a Godfrey Nkhakananga kuti akayimbile masewelo a ndime ya chipulula a mu mpikisano wa World Cup a mchaka cha 2026.

Malingana ndi FIFA, Nkhakananga adzayimbila masewelo a pakati pa Sierra Leone ndi Djibouti omwe adzachitike pa 5 June 2024 pa bwalo la Jadida mu mzinda wa Casablanca mdziko la Morocco.

Oyimbila Nkhakananga akagwira ntchito ya FIFA-yi mothandizana limodzi ndi Clemence Kanduku kuphatikiza Lucky Kegakologetswe ochokera mdziko la Botswana.

Polankhula ndi wailesi ina mdziko muno Mlembi wamkulu wa bungwe la oyimbila la National Referees Association a Chris Kalichelo ati kusankhidwa kwa a Godfrey Nkhakananga ndi a Clemence Kanduku ndi chitsimikizo kuti oyimbila a mdziko la Malawi akwanitsa kunyamula chikhulupiliro cha bungwe lalikulu la FIFA.

Pamene masewelo a M’ndime yachipululayi akakhale ali mkati, nayo timu ya mpira ya Malawi ‘the Flames’ idzakhala ikukumana ndi Sao Tome pa 6 June pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.

Advertisement