Ma khonsolo ambiri akukanikabe kugwiritsa bwino chuma

Advertisement
Dowa District Council

Kafukufuku ataulula kuti khonsolo ya boma la  Dowa ndi yokhayo yomwe yachita bwino pa kugwiritsa  ntchito bwino  ndalama za khonsolo zaonetselatu kuti ma khonsolo ena akukanika.

Malinga ndi kafukuku wa 2024 owona za momwe mankhonsolo akugwiritsila ntchito chuma pa zitukuko zosiyanasiyana zaonetsa kuti khonsolo ya boma la Dowa ndi yomwe ikuchita bwino ndipo achiwiri ndi ma khonsolo a boma la Mchinji ndi Kasungu.

Nduna yowona za maboma ang’ono a Richard Chimwendo Banda ati ngakhale ma khonsolo ena sanachite bwino kweni kweni koma kafukufukuyu wasonyeza kuti ma khonsolo akugwiritsa ntchito bwino  chuma chawo.

Bwanamkubwa wa boma la Dowa a Stallichi  Mwambiwa ati kuchita bwino kwa khonsolo ya boma la Dowa ndi chifukwa cha mgwirizano omwe ulipo pa akuluakulu a khonsoloyi kuphatikiza ogwira ntchito.

Kafukufukuyu wasonyezanso kuti ma khonsolo a ma  boma 7 alibe ndondomeko zovomelezeka zoyendetsela chuma.

Ma khonsolo 21  a ma boma a Dedza, Chitipa, Karonga, Likoma, Mulanje, Mberwa, Nkhotakota, Ntcheu,Blantyre, Salima, Zomba, Chikwawa, Chiradzulu, Lilongwe, Nsanje, Thyolo, Rumphi, mizinda ya Lilongwe, Mzuzu ndi Blantyre ndi omwe ali ndi ndondomeko zakayendetsedwe ka chuma chawo.

Mu Kafukufuku wawo okhudza ma khonsonsolo a Mustafa Hussein  Mphunzitsi wa ku sukulu ya ukachenjede ya University of Malawi (UNIMA) adapeza kuti ma khonsolo ali ndi udindo waukulu pa kayendetsedwe ka chuma cha dziko ndipo kupezeka kwa ma khansala mu ma khonsolo kumathandiza kayendetsedwe kabwino ka chuma cha ma khonsolo.

Advertisement