Anjatidwa pochita malonda ogulitsa munthu

Advertisement
Malawi24

Zina ukamva kamba anga mwala!

A Polisi ku Dwangwa m’boma la Nkhotakota amanga abambo awiri powaganizira kuti amafuna kuchita malonda ogulitsa mwana wam’muna wa zaka ziwiri.

Abambowa ndi a Pilirani Thumba a zaka 38 omwenso ndi bambo ake a mwana ofuna kugulitsidwayu komanso a Yohane Watch a zaka 48.

Ofalitsa nkhani za apolisi ku Dwangwa, a Andrew Kamanga akuti apolisi akwanitsa kugwira anthuwa atatsinidwa khutu ndi anthu ena pamene abambo awiriwa amasakasaka ma kasitomala pa malo ena odyera chakudya.

“Zoona, tinawapeza oganizilidwa mulanduwa mu chipinda china pamene amadikilira kasitomala oti awagule malonda awowa,” adafotokoza Kamanga.

Azibambowa adawatengera ku polisi komwe adawathambitsa ndi mafunso.

Padakalipano, abambowa awatsegulira mulandu ofuna kugulitsa munthu zomwe ndi zosemphana ndi gawo 267 la malamulo a dziko lino.

A Pilirani Thumba amachokera m’mudzi mwa Gobede, mfumu yaikulu Chakhaza m’boma la Dowa ndipo a Yohane Watch amachokera m’mudzi mwa Chatama, mfumu yaikulu Kayembe m’boma lomweli la Dowa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.