Achinyamata tisalore kugwiritsidwa ntchito ndi andale – Msonda

Advertisement
Ken Msonda

Ken Msonda omwe pano adalowa chipani cholamura cha Malawi Congress Party (MCP) achenjedza achinyamata kuti asalore kugwiritsidwa ntchito ndi anthu andale.

A Msonda anayankhura izi pa pologalamu yomwe amapanga ndi nyumba yowulutsa mawu ya PLFM pomwe amayankhura ngati a Think Tank.

M’mawu awo anati pamene nthawi ya zisankho yayandikira, andale ochokera ku zipani zosiyanasiyana amagwiritsa ntchito achinyamata ngati nyambo yokopera anthu kuti apambane pa chisankho zomwe zili zolakwikwa kwambiri.

Iwo anati chomwe aliyense yemwe adakali wachinyamata akuyenera kudziwa panopa n’chakuti anthu andale amangodziwa kugwiritsa ntchito munthu komano vuto likabwera ovutika amakhala makolo ndi achibale ena iwo kulibe.

“Ndiwapemphe achinyamata, tisalorere kugwiritsidwa ntchito ndi anthu andale, chifukwa mukapanga zonsezija akumangani, mupita nokha ku Maula, ana anu, makolo avutika. Amene amakuitanani aja amakhala akuyenderabe galimoto zopuma,” adatero pototokoza.

Iwo atinso atsogoleri andale akuyeneranso kutengapo mbali pothana ndi mchitidwe olimbikitsa ndale zazipolowe zomwe zimayambitsa chidani komanso nkhondo pakati pa anthu otsatira zipani zosiyanasiyana.

A Msonda ati a polisi ngati gawo limodzi la chitetezo, akuyenera kugwira ntchito yawo kwambiri mu nthawi yomwe tikuyandikira zisankho, pofufuza komanso kutsekera mchititokosi aliyense opedzeka akulimbikitsa m’chitidwe wazipolowe.

Pomalidza anapempha a Pulesidenti Lazarus Chakwera kuti ayesetse kupereka uthenga omwe ungadzetse mtendere kwa anthu omwe amatsatira zipani zosiyanasiyana, popeza kupanda kutero zisankho zomwe zikuyembekeredzedwazi kuchitika m’dziko muno zitha kudzakhala zovuta kwambiri.

Msonda ndi mkhalalakale pa nkhani za ndale ndipo iwo anakhalapo m’zipani zosiyanasiyana monga People’s Party(PP) komanso Democratic Progressive Party (DPP).

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.