Mayeso a Pulayimale ayamba bwino mu mzinda wa Zomba

Advertisement
PSLC Exams Zomba

Mayeso a ophunzira a standard 8 omwe akulemba mayeso omaliza opitila ku sukulu za secondary omwe amayendetsedwa ndi bungwe la MANEB, ayamba bwino school za mu mzinda wa Zomba.

Malawi24 itayendera sukulu ya pulayimire ya Bwaila ndi Polisi yapeza ophunzira ali nkati molemba phunziro lachingelezi.

Sister Ruth Kamwendo omwe akuyang’ira mayeso ku sukulu ya Bwaila atiuza kuti ophunzira 126 ndiwomwe akulemba ndipo ndiwochokera sukulu zitatu zomwe ndi Bwaila, Levels ndi Wafwa Pulayimale.

Sister Ruth Kamwendo
Mayeso akuyenda bwino – Kamwendo.

Sister Kamwendo atiuzanso kuti ophunzira m’modzi walephera kuyamba kulemba nawo mayesowa ndipo ati afufuza kuti awone chomwe chachititsa kuti ophunzirayu alephere kubwera.

Ndipo omwe akuyang’anira mayeso pa Polisi Pulayimale, Esther Kanthiti atiuza kuti mayeso ayamba bwino ndipo ophunzira 261 ndiwomwe akulemba ndipo ndiwochokera sukulu ziwiri Polisi ndi Matiya Pulayimale.

Sukulu zonse achitetezo alipo okwanira ndipo palibe cholakwika chilichonse chomwe akumana nacho chokhudza mayeso.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.