Tsiku la 40: Crossroads Hotel yagwidwa ndi zithuzi za zakudya zomwe siinaphike ndiiyo

Advertisement

Ngati muli ndi zithuzi zomwe munajambula zakudya zomwe munaphika nokha ndipo zimaoneka mopatsa mudyo, pansi mtedza; kunjaku kuli Crossroads Hotel (Blantyre) yomwe yayaluka kamba kotenga zithuzi za zakudya zophikidwa kwina mkumati zaphikidwa kwawoko.

Chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke nyanga nchakuti, Lolemba pa 22 April, 2024, tsamba la fesibuku la wayilesi ya Zodiak panaikidwa chithuzi choitanira malonda chomwe eni ake ndi a hotela ya Crossroads yomwe ili munzinda wa Blantyre.

Pachithunzipo panaikidwa zakudya zomwe zimaoneka mowutsa mudyo kwabasi ndipo hotela ya Crossroads imayitana anthu kuti akalawe zakudya zokhetsetsa dovuzo ponena kuti zikumaphikidwa ku hotela kwawo komweko.

Komatu paja akuluakulu akale anati ukatambatamba umayenera kuyang’ana ku m’mawa kuopa kungakuchere; zadziwika kuti zakudyazi zinaphikidwa ku hotela ya Crossroads-yi ndi bodza la mkunkhuniza.

Ngati mbala yomwe imabwera ukugona, eni ake a komwe kunaphikidwa zakudyazi omwe ndi a Max & Sherry Dine and Lounge, anatulukira ndikuulura kuti zakudya zomwe zinaoneka pa chithuzi cha hotel ya Crossroads-zo, anamandwa omwe anazithyakula ndi iwowo.

M’modzi mwa akuluakulu ku Max & Sherry Dine and Lounge a Hope Mezuwa, analemba pa tsamba lawo la fesibuku kuwulura kuti ali ndi umboni onse oti zakudya zomwe Crossroads ikuti ndi zophikidwa ndi iwowo, zinaphikidwa ndi kujambulidwa ndi iwowo.

A Mezuwa anavumbulutsa zithuzi zoyambilira zenizeni zomwe anajambula chakudya chononachi momwe ankamupatsa kasitomala wawo wina yemwe anapita ku malo awo odyerawo omwe ali munzinda omwewu wa Blantyre.

Apa ndi pomwe zinadziwika kuti hotela ya Crossroads inapanga zautsizinamtole, ndipo hotelayi itadziwa kuti yalakwa, inachotsetsa chithuzi choyitanira malonda chomwe chinayikidwa pa tsamba la wayilesi ya Zodiak-cho.

Anthu ena analangiza akuluakulu a malo odyera a Max & Sherry Dine and Lounge kuti akasumile hotela ya Crossroads kamba kaumbavawu, koma mwamwayi a Mezuwa ati akhululukira hotelayi koma isadzayambireso.

Iwo analemba pa tsamba lawo la fesibuku kuti akudziwa kuti ngati angakasumile hotela ya Crossroads, nde kuti munthu wina ntchito yake imuthera zomwe anati sizabwino ndipo alangiza hotelayi kuti itengelepo phunziro.

Pakadali pano akuluakulu a hotela ya Crossroads ya ku Blantyre sanabwere poyera ndikuyankhula pa zomwe zachitikazi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.