“Bodza ili”: Premier Bet yatutumutsa gulu polengeza kuti munthu wawina K639 miliyoni

Advertisement

Anthu m’masamba amchezo ati ndiodabwa kuti kampani yochititsa juga ya Premier Bet yalengeza kuti munthu wina wawina ndalama zokwana K639 miliyoni pomwe malamulo a kampaniyi amati munthu sangawine ndalama zopitilira K500 miliyoni ndipo ena akuti akuona ngati uku nkusatsa malonda chabe.

Lolemba pa 15 April, 2024, kampani ya Premier Bet inalengeza kuti mzika ya dziko la Ethiopia, yomwe ikukhala kumalo osungira anthu othawa kwawo a Dzaleka m’boma la Dowa, yapambana ndalama zokwana K639.4 million.

A Butamo adapambananso mchaka cha 2019.

Kampaniyi inati munthuyu yemwe dzina lake ndi Temesgen Butamo, wa zaka 38, anapambana ndalamazi atalosera molondora masewero a mpira wamiyendo okwana 22 ndipo akuti anagwiritsa ntchito ndalama yokwana K300 yokha.

Koma nkhaniyi yadzidzimutsa anthu ndipo ambiri akuona ngati nkhaniyi ndi bodza la nkunkhuniza ponena kuti malamulo a kampani amati munthu atha ku wina ndalama malire K500 miliyoni.

Anthu ena omwe athilira ndemanga za nkhaniyi kudzera m’masamba a nchezo osiyanasiyana, ati akuganiza kuti kampaniyi yapanga izi ndicholinga chofuna kukopa anthu kuti azipanga nawo juga ku kampaniyi.

“Aaaa asatipusitse awa, izizi ndizopangana cholinga enafeso tigwe mmayesero opanga nawo bet. Kodi mesa chi machine chawo chija chili ndi malire omwe munthu angawine, nde apa zikutheka bwanji, bodza ili, musatinamize,” watelo munthu wina poyikira ndemanga pa tsamba lino la fesibuku.

Munthu wina watiso ndizodabwitsa kwambiri kuti munthuyu wa wina ndalama zosezi kudzera m’masewero a mpira wa miyendo ndipo 11 mwa masewero omwe anabetcha ndi achikho cha English Premier League, zomwe akuti n’zokaikitsa kwabasi kuti munthu angalosere molondora.

“Koma m’mene ikuyendera EPL pano munthu angakwanitse kulosera molondira ma game mpaka 11? Aaaa bodza lenileni ili,” wateloso munthu wina pa tsamba la X mu uthenga omwe unalembedwa nchizungu.

Chinthu china chomwe chadulitsa mutu wa zizwa nchakuti Butamo yemwe wa wina ndalamazi, anawinaso ndalama zokwana 52 miliyoni mchaka cha 2019 zomwe ena akuti mwina nkutheka munthuyu amachita kugwirizana ndi kampaniyi.

Pakadali pano sitinalankhule ndi akuluakulu a kampani ya Premier Bet kuti ayankhe pa funso lomwe anthu akufusa kuti nchifukwa chani munthuyu wapambana ndalama zozyora mlingo omwe unaikidwa wa K500 miliyoni.

Advertisement