Unduna woona za Ulimi watulutsa mitengo yogulira mbewu

Advertisement

Boma kudzera muunduna owona za Ulimi m’dziko muno watulutsa mitengo yoyambira kugula mbewu ya chaka chino ndipo mwazina Chimanga chizigulidwa pamtengo wa K650 pa kilogiramu.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe undunawu watulutsa lachinayi pa 4 April 2024 kudzera kwa mlembi mu undunawu a Dickxie Kampani.

Mitengo yogulira mbewu zina ili motere: Soya K800, Mpunga osapuntha K650, Nyemba zosasakaniza K1200, Nyemba zosakaniza K900, Khobwe K750, Mtedza osaphwanya K800 pa kilo, Mtedza okuswa k1200 pa kilo, Thonje k900, komanso Nandolo k700 mwazina.

Undunawu wachenjezanso anthu onse ogula mbewu kwa alimi pa mitengo yotsika yosemphana ndi yomwe boma lakhazikitsa ponena kuti uwu ndi mlandu waukulu.

Advertisement