Khalidwe ndi chuma: Gaba wanyanyula a Malawi

Advertisement

Nkhani yomwe ili mkamwamkamwa pa masamba a nchezo pakadali pano ndi ya osewera ku tsogolo mutimu ya dziko lino, Gabadinho Mhango yemwe lero watutumutsa anthu pomwe akuoneka kuti sanasangalatsidwe kuti anatulutsidwa m’masewero lero.

Gaba yemwe pano akusewera ku timu ya Moroka Swallows mdziko la South Africa, anali nawo mgulu la osewera omwe mphunzitsi wa timu ya Malawi Patrick Mabedi anaidalira pomwe timuyi imakumana ndi timu ya Zambia mumpikisano wa mayiko anayi omwe ndi Malawi, Zambia, Zimbabwe komaso Kenya.

Mchigawo choyamba, Gaba sanawonetse zintchito zotamandika zomwe a Malawi ambiri akumudziwa nazo komabe mphunzitsi Mabedi sanamutulutse osewerayu kufikira kumapeto kwa chigawo choyamba chomwe timu ya Flames inali ikutsalira ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi.

Chigawo chachiwiri chitangoyamba kumene, Gaba anatulutsidwa m’masewelowa pamodzi ndi Lloyd Njaliwa komaso Patrick Mwaungulu ndipo izi zikuoneka kuti osewerayu sanagwilizane nazo.

Chapatali, Gaba amaoneka akuyankhula mokwiya kusonyeza kuti wanyasidwa ndi chiganizo cha kutulutsidwa kwake komaso pamwamba pa zonsezo, mmalo mopita pa malo pamene pamakhala osewera omwe atulutsidwa, iye anatuluka m’bwalori ndikupita chindunji ku chipinda chomwe osewera amavalira.

Khalidwe lomwe Gaba waonetsa likuoneka kuti silinasangalatse a Malawi ochuluka omwe ambiri mwa iwo alemba m’masamba a nchezo kuti osewerayu sanachite bwino ndipo ena akuti katswiri omwetsa zigoliyu akoze khalidwe lake.

“Patson Daka watulutsidwa sananyanyale wakhala pa bench. Gaba watulutsidwa koma kunyanyala uku akulalata kupita ku dressing room. Gaba amazimva kuti anafikapo eti? Asatitopese,” watelo munthu wina polemba patsamba lake la fesibuku.

Anthu ena ati khalidwe longa ililili ndikuthekera komuwonongera tsogolo osewerayu poti paja amati khalidwe ndi chuma komaso ena ati izi mwina zingachotse chidwi cha mphunzitsi wa timuyi kuti azamuyitaneso osewerayu ku tsogoloku.

“Mwamuonatu Gaba wanuyu, uyuyu khalidwe alibe, ndipo nkanakonda coach asazamuitaneso ndithu chifukwa nde zomwe wapangazi aaaa sizoona. Izi nde zikumuononga munthuyu,” wateloso munthu wina pa fesibuku.

Mbali inayi, anthu ena ati sanaone vuto lili lonse pa zomwe Gaba anapanga ndipo enaso akuloza chala mphunzitsi Mabedi ponena kuti sisitimu ya kaseweredwe yomwe amagwiritsa ntchito pa masewero alero siinali bwino.

“Ine ndikuona ngati coach team yankukulira, system imene wamenyetsa mabedi ndi yomuonetsa player ngati osatatha, how can you play with a single striker and mipira yobwera ndikukhala zamwamba yet the striker is short. Will you expect miracle in that situation and the player was not bad at all even ndili ine ndizobowa,” waikiraso mlomo munthu wina pa tsamba lina pa fesibuku.

Chaka chatha, mphunzitsi Mabedi sanamuitane Gaba pa masewero angapo omwe timu ya dziko lino imasewera kamba koti anathawidwa ndi ndege pomwe amayembekezeka kubwera kuno kuchoka mdziko la South Africa ndipo izi zitachitika, anthu anayankhula zambiri kumunyoza Mabedi kamba komusiya osewerayu.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.