Thambo lagwa Ku Nigeria pamene katswiri opanga kanema wazisudzo watisiya

Advertisement

Mdima wagwanso m’dziko la Nigeria pamene katakwe opanga mafilimu yemwe dzina lake ndi Amaechi Mounagor wadziwika kuti wamwalira atadwala nthenda ya impso.

Izi zikudza pasanathe mwezi dzikoli litatayanso katswiri wina a John Okafor yemwe amadziwika bwino ndi dzina loti Mr Ibu kumayambiliro a mwezi uno.

Mmasiku apitawo a Mounagor adabwera poyera kwa anthu aku Nigeria kupempha thandizo la ndalama pofuna kuti apite ku India kuti akalandire chithandizo.

Malemuwa adatchuka kwambili kudzera mu kanema wotchedwa ‘Aki na Ukwa’ yemwe adatuluka mchaka cha 2003.

A Mounagor amwalira ali ndi zaka 61, ndipo awa ndi mafilimu ena omwe iwo alimo: Most Wanted Kidnappers (2010), My Village People (2021), Aki na Ukwa (2003), Guardian Angel komanso Evil World yomwe idatuluka mchaka cha 2015 ndi ena ambiri.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.