Phi!! Yagwanso Malawi Kwacha

Advertisement
Money currency

Nyimbo yake mwina nkukhala ya “timalizeni, tatsala pati?” kapena mwina ija ya pa mauthenga a chisoni ya “Atimwe”. Banki yaikulu ya mu dziko muno yaswa nkhonya ina yowawa: Malawi Kwacha yagwanso.

Malinga ndi chikalata chimene bankiyi yatulutsa, iwo ati pa malonda a msinthano amene anachititsa zaoneka kuti Kwacha tsopano yagwa ndi 3 Kwacha pa 100 Kwacha iliyonse (3 peresenti).

Malinga ndi chikalatachi chomwe asayinira a Wilson Banda, mtengo ovomerezeka ogulitsira ndalama ya Kwacha mosinthana ndi dollar ya ku Amereka tsopano ndi MK1,751.

Koma a katswiri a zachuma ati kugwetsa kwa ndalamayi sikuti kukulinganizana ndi mtengo wache weniweni. Iwo ati mtengo weniweni wa ndalama ya dollar ya ku Amereka mofanizira ndi Kwacha ukudutsa MK2, 000.

Kugwetsa kwa ndalama ya Kwacha kwadza pomwe dziko lino likusowa zinthu monga sugar komanso mitengo yake ikunka ikukwera. Anthu ochita malonda akhalanso akudandaula kuti ndalama ya m’maiko akunja yochitira malonda sikupezeka.

Advertisement

One Comment

Comments are closed.