Chaka chilichonse pa 24 March ndi tsiku lomwe dziko la Malawi limakhala likukumbukira Matenda achifuwa chachikulu cha TB ndinso matenda a Khate, ndipo chaka chino mwambo okumbukira tsikuli ukachitikira m’boma la Mulanje.
Malingana ndi mlembi Wankulu mu Unduna wa za Umoyo Dr Samson Mndolo, mutu wa chaka chino ndi wakuti ‘Zowonadi tikhoza kuthetsa TB, tigonjetse TB kuti matendawa akhale mbiri yakale’, komanso mutu wa Khate ndi wakuti ‘Tigonjetse Khate’.
A Mndolo ati pamene kwangotsala zaka zisanu ndi chimodzi zokha kuti tifike m’chaka cha 2030 chimene tiri ndi chiyembekezo chothana ndi TB, 2024 ndi chaka chofunikira kwambiri kuti anthu a dziko lino agwirane manja kuti pofika 2030 matendawa akhale mbiri yakale.
Iwo awonjezera ponena kuti dziko lino ladzipereka pofuna kuthana ndi Matenda a TB pokhazikitsa ndondomeko zothetsera matendawa mogwirizana ndi bungwe la za Umoyo pa dziko lonse la pansi limene likulimbitsa kuchepetsa infa zobwera chifukwa cha TB.
“Chinanso tiwonetsetse kuti anthu amene ali ndi Matenda a Khate akulandira ulemu moyenerera. Boma likuwonetsetsanso kuti mzipatala zonse muli anthu wogwira ntchito, zipangizo zoyenera matendewa, mankhwala ndi zina zofunikira zikupezeka”, watero Mlembiyu.
A Mndolo apempha atsogoleri onse andale, amabungwe, abwenzi amene amathandiza pa chuma ndi ena onse kuti atenge mbali pofalitsa uthenga wa TB komanso Khate.
Iwo atinso ndi udindo wa aliyense kutengapo mbali pofalitsa uthenga wa TB kuti anthu azipita ku Chipatala mwansanga akawona zizindikiro monga kukhosomola, kutentha thupi, kutsika sikero ndi kutuluka thukuta usiku angakhale kuzizire.
Malingana ndi kafukufuku amene adachitika m’dziko muno m’chaka cha 2014 adasonyeza kuti pa anthu 100,000 alionse , anthu 334 anali ndi TB.
Kafukufukuyu adasonyezanso kuti abambo ambiri ndi amene akudwala TB kusiyana ndi amayi komanso chiwerengero cha anthu odwala TB ndi chokwera kwambiri mma tauni kusiyana ndi m’midzi.