Shado wa DPP wapatsidwa belo kutsatila kumangidwa kwake atauza anthu kuti asalole MCP kufika ku Phalombe

Advertisement

Pomwe anthu omwe anaononga katundu wa chipani cha DPP ndikuvulaza mamembala ena a chipanichi ku Lilongwe sanamangidwebe mpaka pano, apolisi ku Phalombe dzulo anathila unyolo membala wa chipani cha DPP yemwe akufuna kudzapikisana nawo pa mpando wa phungu kum’mwera kwa bomalo, kamba kouza otsatira chipanichi kuti ku Phalombe ndi kwa DPP ndipo asalore chipani cha MCP kufikako.

Padakali pano, khoti ku Phalombe latulutsa mayiyu, yemwe wazindikilidwa ngati Tiaone Hendele, pa belo litamulamula kupereka K100, 000 pompopompo komanso chikole cha K500, 000.

Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi a mchigawo cha kum’mwera chakumvuma a Edward Kabango, Hendele anamangidwa Lolemba ati kaamba komema anthu kuti asalole kongelesi (MCP) kufika ku derali.

A Kabango awuza nyumba zina zoulutsira mawu m’dziko muno kuti a Hendele anapalamula mlanduwu lachinayi sabata yatha pomwe amayankhula pa zochitika zina ku delaro koma ati amangidwa dzulo Lolemba pa 11 March, 2024.

Apolisiwa ati amanga mayiyu kamba koti zomwe adalankhulazo zili ndi kuthekera kobweretsa chisokonezo m’boma la Phalombe ndipo ati anthu enaso akuyenera kutengerapo phunziro.

Mu kanema yemwe anthu akugawana m’masamba a mchezo, a Hendele adauza anthu ku dela lawo kuti pakakhala zochitika zili zonse kuphatikizapo maliro, asamalore akuluakulu a chipani cha MCP kutenga nawo gawo.

Iwo analangiza anthuwo kuti akafika pa zochitikazo adzichita ngati asuta chamba potchingira ma membala a MCP ponena kuti bomali ndi gawo la chipani cha DPP kotelo kuti MCP siyikuyenera kupatsidwa mpata.

“Muonetsetse kuti mwamanga kuti Congress isalowe. Pamene mwamva kuti kudera kwachitika zovuta, tanyamulanani ma area chairman mukamange kumene kuja kuti wa Congress asapezeke. Kaya simunagone tsiku limenelo, tenganani ndi a azimayi omwe, tikafika pa maliro paja tidzikhala ngati tasuta chamba. Asapeze mpata ku Phalombe South, boma la Phalombe si la Congress ndi la DPP,” anatelo mayi Hendele poyankhula pa zochitikazo.

Mayi Tiaone Hendele omwe ndi a zaka 43 ndipo akuyembekezeka kuyankha mlandu woyankhula zinthu zomwe zingathe kubweretsa chisokonezo. Iwo ndi ochokera m’mudzi wa Mangoza kwa Mfumu Yaikulu Nkhumba m’boma la Phalombe lomweli.

Advertisement