Anyamata akuthamanga kuposa Kalulu munzinda wa Mzuzu lero

Advertisement

Mpikisano othamanga wa Mzuzu City Half Marathon wayambika pamene ma athletes ayamba kuthamanga mtunda okwana 21 kilometres kuchokera pa St John’s munzinda wa Mzuzu.

Kuno kuli liwiro lamtondo wadooka pamene anyamata komanso asungwana akulikumba liwiro kuposa kalulu, inde inu kuli kuthamanga kuposa galimoto.

Ma athletes omwe analembetsa mu mpikisano umenewu ndi oposa 130 ndipo kuyelekeza ndi omwe adalembetsa ulendo watha ulendo uno ma athletes omwe alembetsa chaka chino ndi ochulukirapo ndithu.

Ndipo amene apambane pakuthamanga kuposa ena onse apita ndi ndalama zokwana 1.5 miliyoni kwacha kumbali zonse amuna ndi akazi.

Pamene amene akhale pa namba yachiwiri apita ndi ndalama zokwana 1 miliyoni kwacha.

Mpikisanowu wakonzedwa ndi a Malawi National Council of Sports.

Advertisement