Avocado watulutsa nyimbo yatsopano

Advertisement

Oyimba amene sachita manyazi kuyika mimba yake pa mtunda pa masamba a mchezo, Avokado watulutsa nyimbo yatsopano yotchedwa ‘Msandipitilire’.

Avocado yemwe dzina lake lenileni ndi Christopher Malera yemwenso amadziwika ndi dzina loti Amapiano Landlord waimba nyimboyi mothandizana ndi Ethel Kamwendo komanso Temwa.

Avokado mokuwa ndi mawu ake okhakhala nyimbo kungoyamba amvekere ‘aya! ya! ya! ya! Chaka chino chokha ambuye musandiipitilire’.

Zimamveka ngati akudutsa munyengo zokhoma koma iye wati ayi ndi mawu a m’baibulo omwe akuchokera pa Genesis 18 ndime ya 3, amene mumawerenga baibulo mukudziwa zomwe ndimeyi imakamba.

Mawu anthetemya a Dr. Ethel Kamwendo Banda komanso msungwana Temwa apangitsa nyimboyi kuti ibebe chifukwa ikukondedwa ndi anthu akulu komanso achichepere.

“Ndipo sindinati chaka chino nditulutsa nyimbo zakathithi zotumikira yehova koma zoyimbidwa mu chamba cha Amapiano,”anatero avokado mwathamo.

Advertisement