Anthu atatu apezeka ndi nthenda yofilitsa maso ku Blantyre

Advertisement

Anthu atatu apezeka ndi nthenda yofilitsa maso yomwe muchingerezi imatchedwa
conjunctivitis kapena kuti pink eye mu mzinda wa Blantyre.

Malingana ndi kalata yomwe atulutsa owona zaumoyo komanso chisamaliro cha anthu m’bomali, ndipo yasainidwa ndi Dr Gift Kawalazira, m’modzi mwa anthuwa wapezeka pa chipatala chaching’ono cha Chilomoni ndipo ena awiri pa chipatala cha Kadidi.

Kalatayi yapitiliza kunena kuti anthuwa anadutsira m’boma la Karonga komwe mthendayi ikufala kwambiri.

Unduna wa zaumoyo wati anthu oposera 700 m’dziko muno ndi omwe apezeka ndi mthendayi yomwe ndi yopatsirana.

Akatswiri azaumoyo akhala akulangiza anthu kuti azisamba mmanja ndi sopo pafupifupi komanso apewe kugwira mmaso ngati zina mwanjira zopewera kufala kwa mthendayi ndipo apempha boma kuti liphunzitse anthu zambiri zokhudza mthendayi.

Advertisement