Apolisi anjata mayi wina kamba kowotcha mamuna wake ndi madzi otentha

Advertisement

Bambo wina wazaka 41 zakubadwa m unzinda wa Lilongwe ku Nsungwi, ali mu ululu mkazi wake atamuthira madzi otentha pamimba ndipo pakadali pano mkaziyu akusungidwa mchitokosi cha apolisi kaamba kochita zaupanduzi.

Mkaziyu yemwe dzina lake ndi mayi Promise Kamtepa wazaka 21 zakubadwa adathira madzi otentha dzulo amuna awo a Limbikani Mulota pamimba pamene amuna awo amafuna kugwilitsa ntchito kapu ya mayiyo zomwe zidakwiyitsa mayiyu.

Malingana ndi mneneri wa apolisi ya Kanengo a Greciam Ngwira, awiliwa adali atasiyana kale mwezi watha ngati banja angakhale kuti iwo amakhalabe nyumba imodzi koma aliyense akupanga zayekha.

Izi zitachitika anthu ena anathamangira kuchipatala cha ku 25 ndi bamboyu komwe iye akulandira thandizo la mankhwala.

Pakadali pano mayiyu amutsekulira mulandu ovulaza munthu ndipo posachedwapa akaonekera kubwalo la milandu komwe akayankhe mulanduwu.

Mayi Promise Kamtepa amachokera m’mudzi mwa Kathewera kwa mfumu yayikulu Chipeni m’boma la Dowa.

Advertisement