Kampani ya Nacala Logistics yakweza mitengo yonyamulira anthu pasitima

Advertisement

Malingana ndi kukwera kwa zinthu zosiyanasiyana mdziko muno, nayo kampani ya Nacala Logistics yalengeza kuti yakweza mitengo yonyamulira anthu pa sitima ndipo mitengo yatsopanoyi iyamba kugwira ntchito pa 1 March chaka chino cha 2024.

Kampaniyi yanena izi mumkalata yomwe kampaniyi yatulutsa ndipo yati kukwera kwa mitengoku ndi kaamba kakukwera kwa katundu osiyanasiyana m’dziko muno.

Malingana ndi kampaniyi, ina mwa mitengoyi pa business coach ili motere Limbe-Blantyre K650, Limbe-Balaka K4400, Limbe-Liwonde K4400, Limbe-Nayuchi K7350, Blantyre-Balaka K3750, Blantyre-Liwonde K4200, Blantyre-Nayuchi K6500, Balaka-Nayuchi K4400 Balaka- Liwonde K1600, komanso Liwonde-Nayuchi K2950.

Pamene mitengo ya Premier Coach ili motere: Limbe-Blantyre K400, Limbe-Balaka K3150,Limbe-Liwonde K3150, Limbe-Nayuchi K5250, Blantyre-Balaka K2750, Blantyre-Liwonde K2750, Blantyre-Nayuchi K5000, Balaka-Nayuchi K3150, Balaka- Liwonde K150, komanso Liwonde-Nayuchi K2250,

Wolemba: Ben Bongololo

Advertisement