Bambo amafuna kugulitsa mwana pa mtengo wa K7 miliyoni


Bambo wina ku wa zaka 24 wamangidwa ku Kasungu kamba koguna kugulitsa mwana wake pa mtengo wa K7 miliyoni.

Bamboyu yemwe dzina lake ndi Noel Kanyama amafuna kugulitsa mwana wake kwa mkulu wina ochita malonda mtauni ya Kasungu.

Mneneri wa apolisi ku Kasungu a Joseph Kachikho wati anayimbira foni wa malondayo kuti ali ndi mwana wa chaka ndi miyezi isanu ndi itatu yemwe akufuna amugulitse.

Kanyama amati akufuna ndalamayo awonjezere mpamba wa bizinezi yake.

Mkulu wa malondayo anavomela koma anadziwitsa apolisi za nkhaniyi.

Pomwe Kanyama amati akukakumana ndi wamalondayo pa malo ena, anakapezapo apolisi omwe anamunjata.

Bamboyu wauza apolisi kuti iye adalota maloto oti apereke mwanayo nsembe ndi chifukwa chake anaganiza zomugulitsa

Kanyama amutsekulira mlandu ogulitsa ofuna mwana ndipo akaonekela ku bwalo la milandu.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.