Adandaula ndi mchitidwe odula mitengo mwa chisawawa ku Machinga

Advertisement
Malawi Machinga

Akulu akulu a boma la Machinga ati mitengo yomwe inali pa malo okwana mahekitala okwana 50 mu nkhalango zosiyasiyana yadulidwa mu zaka wiri zapitazo.

Wapampando mu khosolo ya Machinga, Cydreck Stande, anati mchitidwewu ukupitilila kamba kakuchepa kwa chitetezo mu nkhalangozi zimene zikupereka mpata kwa anthu ozungulila kuti adzilowa ndi kudula mitengo kuti adziwotchera makala zomwe ndi zoletsedwa ndi malamulo a dziko lino.

Iwo apempha boma kuti lipereke chilolezo ku ma khosolo kulemba alonda oti aziyang’anira nkhalango za maboma ndi cholinga choti nchitidwewu uchepe.

A Stande amayankhula izi pa mwambo okhazikitsa ntchito yobzala mitengo pa sukulu ya primary ya Chinguni ndipo anatiso mapiri a Molina, Chihala ndi Liwonde ndi amene mitengo yadulira yochuluka.

Mkulu wa bungwe la Action in Relief and Development (Card), Clement Musipa ati, izi zikudza kamba ka umphawi, ndipo apempha adindo kuti athandize anthuwa kuwapatsa njira zopezera ndalama zodalilika ngati njira imodzi yochepetsa kudula mitengo mwa chisawawa.

Boma la machinga lili ndi chiyang’aniro chobzala mitengo yosachepera 1.5 miliyoni chaka chino.

Wolemba: Peter Mavuto

Advertisement