Pamene nyumba ya malamulo ya dziko lino yatsala ndi masiku wochepa kuti iyambe zokambirana zake, pali kuthekera kuti zokambirana mnyumbayi zitha kukhala zovuta.
Izi zili chomwechi kutsatira chiganizo chomwe Sipikala wa nyumbayi a Catherine Gotani Hara molangizidwa ndi mkulu wa zamalamulo ku boma a Thabo Nyirenda apanga posavomereza kusankhidwa kwa a George Chaponda ngati mtsogoleri wa otsutsa kunyumba ya malamulo.
Chipani chachikulu chotsutsa cha cha Democratic Progressive (DPP) china anthu ena mchipanicho ndipo mmodzi mwa iwo ndi a Kondwani Nankhumwa womwe anali mtsogoleri wotsutsa kunyumba ya malamulo.
Chipanichi chinasankha a Dr George Chaponda pa undindo wa mtsogoleri wotsutsa boma.
Kudzera mukalata yake, DPP inadziwitsa sipikaa wa nyumba ya malamulo Catherine Gotani Hara. Ndipo Pa 29, January,2024, Sipikala wa nyumba yamalamuloyi anaziwitsa chipani cha DPP kuvomeleza za kusankhidwa kwa a Chaponda ngati mtsogoleri wa wotsutsa ndipo iwo anafunilaso mafuno abwino a Chaponda posankhidwa pa udindowu.
Ndipo kalatayo inapitiliza kupempha a Chaponda kuti akupemphedwa kudzakhala nawo pa zokambirana za komiti yayikulu yowona zokambirana za aphungu mnyumbayo womwe uzakhalepo lachiwiri pa 6 February 2024 nthawi ya 9:30 Mamawa.
Koma maloya a Nankhumwa analembela ofesi ya sipikala kuti a Nakhumwa akadalibe pa udindo wawo ngati Mtsogoleri wotsutsa boma ndiye kuvomeleza a Chaponda kukhala kuphwanya malamulo.
“Mukudziwa kuti pali chiletso chomwe a Nankhumwa anakatenga ku bwalo la milandu m’mbuyomu chomwe sichinachotsedwe, kotero kuvomereza a Chaponda kukhala kudelera khoti lomwe linapereka chiletsocho, panthawi ya m’mbuyomu,” anatelo woyimilira a Nankhumwa.
Ndipo Mlangizi wa boma pa zamalamulo a Thabo Chakaka Nyirenda alangiza sipikala wa nyumba ya malamulo, kuti ofesi yake isavomeleze a Chaponda ngati mtsogoleri watsopano wa mbali yotsutsa.
Koma akatswiri pa nkhani za ndale ndi malamulo akuti a Nankhumwa sali woyenera kukhala mtsogoleri wotsutsa boma mnyumbayo ponena kuti chipani ndichomwe chili ndi mphamvu yosankha mtsogoleri wotsutsa.
Akatswiriwo alangiza a Nankhumwa kuti avomeleze kuti iwo simembelaso wachipani cha DPP.
Koma katswili wina pa za malamulo George Jivason Kazipatike wati ngati kubwalo la za milandu kuli chiletso ndiye kuti a Nankhumwa akadali mtsogoleri wotsutsa. A Kazipatike ati chipani cha DPP chiyenera kukachotsa chiletsocho.
“Ndisimike pano kuti ndizoona kuti chipani chili ndi mphamvu zosankha mtsogoleri wotsutsa mnyumba ya malamulo ndipo chipanicho posankha a Chaponda sichinalakwe” anatero a Kazipatike poyankhula ndi Malawi24.