Chaka chamawa ndilipo pa ballot paper – Nankhumwa


Kondwani Nankhumwa

Inu nonse amene mukutangwa ndikumalemba kuti APM my vote, kapena Chakwera my vote, dziwani kuti mpikisano opita ku state house ukupita kotenthera. Nawo a Kondwani Nankhumwa amene anapitikitsidwa ku chipani cha DPP alonjeza kuti muwaona akupikitsana nawo pa masankhowa.

Polankhula kwa anthu amene akuti ndi owatsatira mu mzinda wa Ndirande, a Nankhumwa ati iwo adachotsedwa mu chipani cha DPP chifukwa amafuna kukapikisana ndi a Mutharika.

“Ine anandichotsa chifukwa ndimafuna kukapikisana nawo ku konveshoni ya DPP,” anatelo a Nankhumwa.

Iwo anatambasulanso kuti zimene zakhala zikutchuka kuti alowa ku Kongeresi kapena UTM ndi zabodza.

“Ine sindinayankhulepo pa kuchotsedwa kwanga, ndikazayankhula dziko lonse lizagwedezeka,” anatero a Nankhumwa.

Ngakhale sadafotokoze ngati iwo ayambitse chipani chawo kapena kulowa zipani zimene zilipo kale, iwo atsindika kuti pa mndandanda wa anthu ozayima 2025, nawo ali pompo.

A Nankhumwa amene lero adali mlendo olemekezeka pa mwambo okhazikitsa m’busa watsopano pa mpingo wa CCAP ku Ndirande Makata adachingamiridwa ndi achinyamata amene anavala makaka a chipani cha DPP.

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.