Mapasipoti akukanika kutuluka ku Immigration

Advertisement
Malawi passport

Mavuta akuwoneka kuti sakutha ku nthambi yowona za anthu olowa ndi kutuluka m’dziko muno (immigration) pomwe nthambiyi yati ikukanika kutulutsa ziphaso zoyendera (Passport).

Izi ndi malingana ndi uthenga wa nthambiyi kupita kwa a Malawi wati.

“Tikuziwitsa a Malawi kuti makina athu wotulutsira ziphatso zoyendera (Passport) ali ndivuto ndipo pakadali pano sitikutulutsa ziphasozi koma anthu athu okonza ali mkati mokonza makinawa ndipo zikatheka tikudziwitsani,” yatero mbali ya uthengawo.

Nthambiyi yakhala ikukumana ndimavuto ena pomwe nthambiyi inazayimitsapo kutulutsa ziphaso ponena kuti imakonza kaye ndondomeko zatsopano

Chithetsereni kontirakiti ndi kampani yomwe imasindikiza passport nthambiyi, yakhala ikukumana ndizovuta zambiri, pomwe anthu akhala akudandawula kuti nthambiyi ikumachedwa kwambiri kutulutsa ma passport.

Mwachitsanzo passport ya MK90,000 ikuyenera kuti mumasiku khumi (10) ikhale itatuluka pomwe passport ya MK180,000
Ikuyenera kuti izituluka m’masiku atatu (3) koma izi sizikumakhala chocho.

Advertisement