Pulofeti ochita za akuluakulu ndi mwana wake uja wagamulidwa zaka 19


Prophet Christopher Phiri (L) at a court in Zomba

Mneneri Christopher Phiri wa zaka 40 yemwe ndi mwini utumiki wa Supernatural Embassy ku Mangochi, wagamulidwa kukaseweza jere zaka khumi, mphambu zisanu ndi zinayi (19) kamba koseweretsa malo obisika a mwana wawo wa mkazi wa zaka 16 zomwe akuti zinali ndi kuthekera koti anakatha kugonana naye.

Ngakhale Phiri aloza chala mwana wawoyo kuti anachita kuwaputa dala, khothi silinamve ndipo lawamula kuti akaseweze.

Pomwe mlanduwu umavedwa, mkulu oyimilira mbali ya boma pa mlanduwu a Inspector Amos Mwase pamodzi ndi Brenda Khwale, yemwe ndi loya wa Centre for Human Rights, Education, Advice and Assistant and Rehabilitation (CHREAA), adauza khoti kuti Phiri anachita mwikhowu pakati pa mwezi wa September ndi November, 2023, mmudzi mwa Kela mfumu yaikulu Mponda ku Mangochi.

Inspector Mwase anauzaso khothi kuti mtsikanayu poyamba amakhala ndi mayi ake potsatira kutha kwa banja la makolo ake pomwe iye anali ndi zaka ziwiri ndipo akuti mu September chaka chino, bambo Phiri anamuitana mwana wawoyu kuti adzikhala naye kunyumba kwawo ndipo mkati mokhala naye, anthu anayamba kudabwa ndi m’mene bamboyu amakhalira naye mwana wakeyu.

Khothi lidamvanso kuti kumayambiriro kwa mwezi wa November, mphekesera zidayamba kumveka kuti mtsikanayu amakakamizidwa kugwira ntchito ya nzimayi pakhomo la bambo akelo ndipo pa November 28, apolisi adadziwitsidwa ndi anthu ammudzi za momwe awiriwa amakhalira zomwe akuti zidawapangitsa kuti apolisiwo awayitane awiriwa padera kuti akawafunse mafunso.

Atayitanidwa ku polisi, zidadziwika kuti mphekeserazo zinali zoona kamba koti apolisi anapeza zithunzi zamaliseche ndi mavidiyo olaula za bamboyu ndi mwana wakeyo m’mafoni awo a m’manja zomwe zinapangitsa kuti mkuluyu amangidwe.

Atakaonekera kubwalo la milandu, Phiri yemwe ankayimiridwa ndi Counsel Smart khalifa, adavomera mlandu wochita zosayenera ndi mwana komanso kuchitira nkhanza mopanda ulemu mwana wawoyu.

A Phiri anapempha khothi kuti liwachitire chifundo ponena kuti ndikoyamba kulakwa komaso iwo analoza chala mwana wawo wamkaziyu ponena kuti anawakopa kuti achite naye zosayenera.

Koma popereka chigamulo, Senior Resident Magistrate Muhammad Chande, adagwirizana ndi oyimilira boma pa mlanduwu za kufunika kopeleka chilango chokhwima kwa bamboyu ponena kuti likhale phunziro kwa azibambo ena amalingaliro olakwika ngati awa.

Pachifukwa chimenecho, a Chande alamula kuti mneneri Phiri akaseweze jere kwa zaka 19 chifukwa chochita zosayenera ndi mwana wachichepere komanso zaka 13 chifukwa chozuza mopanda ulemu mwana koma zigamulozi ziziyenda nthawi imodzi zomwe zikutanthauza kuti a Phiri akakhala kundende zaka 19 osati zaka 32.